ebook img

Mapazi Opita Kwa Kristu PDF

91 Pages·0.478 MB·Bulgarian
Save to my drive
Quick download
Download
Most books are stored in the elastic cloud where traffic is expensive. For this reason, we have a limit on daily download.

Preview Mapazi Opita Kwa Kristu

Mapazi Opita Kwa Kristu Ellen G. White Copyright © 2014 Ellen G. White Estate, Inc. Information about this Book Overview This eBook is provided by the Ellen G. White Estate. It is included in the larger free Online Books collection on the Ellen G. White Estate Web site. About the Author Ellen G. White(1827-1915)isconsideredthemostwidelytranslated American author, her works having been published in more than 160 languages. She wrote more than 100,000 pages on a wide variety of spiritual and practical topics. Guided by the Holy Spirit, she exalted Jesus and pointed to the Scriptures as the basis of one’s faith. Further Links A Brief Biography of Ellen G. White About the Ellen G. White Estate End User License Agreement The viewing, printing or downloading of this book grants you only a limited, nonexclusive and nontransferable license for use solely by you for your own personal use. This license does not permit republication, distribution, assignment, sublicense, sale, preparation of derivative works, or other use. Any unauthorized use of this book terminates the license granted hereby. Further Information For more information about the author, publishers, or how you can support this service, please contact the Ellen G. White Estate at [email protected]. We are thankful for your interest and feedback and wish you God’s blessing as you read. i MAU OYAMBA M’mapirikaniro ambiri mumamveka kuitana kwa mtengo wap- atari, “Idzani kuno kwa Ine,”—kuitana kwa Mpulumutsi wacifundo amene mtima wace wa cikondi umapita kwa onse amene ali ku- socera kulekana ndi Mulungu; ndipo m’mitima ya ambiri amene ali kulakalakadi cithangato ca kupeza Yesu, mumauka cifuniro ca kub- werera ku nyumba ya Atate. Oterewa kawiri kawiri amabwerezanso cifunso ca Tomasi, “Tidzadziwa njira bwanji?” Nyumba ya Atate iyang’anika ngati iri kutari, ndipo njira yace iwoneka yobvuta ndi yosadziwika. Nanga mapazi ace ngotani amene amatsogolera njira ya kunka kwathu? Dzina la bukhuli lifotokoza nchito yace. Limasonyeza kwa Yesu kuti ndiye yekha angathe kukwanitsa zosowa za moyo, ndi kutso- golera mapazi okaika ndi otsimphina ku “njira ya mtendere.” Li- matsogolera wofuna cilungamo ndi makhalidwe amphumphu, phazi limodzi limodzi m’njira ya moyo wa Cikristu, ku cidzalo ca dal- itso cimene cimapezeka m’kudzipereka kotheratu ndi cikhulupiriro cosagwedezeka m’cisomo copulumutsa ndi mphamvu ya kusunga ya Bwenzi la ocimwa. Malangizo opezeka m’bukhu ili anatengera cisangalatso ndi ciyembekezo ku miyoyo yambiri yobvutika, ndipo lathangata otsata Yesu ambiri kuyenda molimbika ndi mokondwa m’mapazi a Mtsogoleri wawo wa kumwamba. Tiri kuyembekeza kuti lidzanyamula uthenga womwewu kwa enanso ambirimbiri amene ali kusowa cithangato comweci. “Njira iwonekere Makwerero opita kumwamba.” Zinali cotero ndi Yakobo, pamene, atapanikizidwa ndi mantha kuti chimo lace lamlekanitsa ndi Mulungu, iye anagona kupumula, ndipo “analota, ndipo taonani makwerero anaima pa dziko, ndipo pamwamba pace panafika kumwamba.” Motero cilumikizano ca kumwamba ndi dziko lapansi cinaululidwa kwa iye, ndipo mau a ii cisangalatso ndi ciyembekezo analankhulidwa kwa woyendayo ndi Iye amene anaima pamwamba pa makwererowo. Masomphenya a kumwambawa abwerezedwenso kwa ambiri pamene ali kuwerenga nthanoyi ya njira ya moyo. OSINDIKIZA. [5] Contents Information about this Book . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . i MAU OYAMBA . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . ii MUTU 1—CIKONDI CA MULUNGU KWA MUNTHU . . . . . . 5 MUTU 2—WOCIMWA ASOWA KRISTU. . . . . . . . . . . . . . . . . 11 MUTU 3—KULAPA . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . 15 MUTU 4—KUBVOMEREZA . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . 25 MUTU 5—KUDZIPEREKA . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . 29 MUTU 6—CIKHULUPIRIRO NDI KULANDIRIDWA . . . . . 34 MUTU 7—YESO LA KUKHALA WOPHUNZIRA WA YESU 39 MUTU 8—KUKULA KUFANANA NDI KRISTU . . . . . . . . . 46 MUTU 9—NCHITO NDI MOYO . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . 53 MUTU 10—KUDZIWA MULUNGU . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . 58 MUTU 11—UBWINO WA PEMPHERO . . . . . . . . . . . . . . . . . 64 MUTU 12—COCITA NAKO KUKAIKA . . . . . . . . . . . . . . . . . 73 MUTU 13—KUKONDWERERA MWA AMBUYE . . . . . . . . 79 iv MUTU 1—CIKONDI CA MULUNGU KWA MUNTHU Cilengedwe ndi cibvumbulutso zimacitira umboni za cikondi ca Mulungu. Atate wathu wa kumwamba ndi kasupe wa moyo, wa nzeru, wa cimwemwe. Taonani zinthu zozizwitsa zokometsetsa za cilengedwe. Taganizani za nchito zace zozizwitsa pa kukwanitsa zosowa ndi cikondwerero ca anthu ndi ca zolengedwa zonse. Dzuwa ndi mvula, zimene zimakondweretsa ndi kutsitsimutsa dziko, mapiri ndinyanjandimadambo, zonsezizimatiuzaifezacikondicaMlengi. Amene amakwanitsa zosowa za zolengedwa zace ndiye Mulungu. Davide ananena mau okometsetsa otere, — “Maso a onse ayembekeza Inu ndipo muwapatsa cakudya cawo m’nyengo zawo. Muolowetsa dzanja lanu, nimukwaniritsira za moyo zonse cokhumba cawo.” Salmo 145: 15, 16. Mulungu anapanga munthu woyera mtima ndi wokondwa; ndipo dziko lokongola pamene linaturuka m’manja a Mlengi linalibe kadonthokobvundakapenamthunzi watemberero. Cimenecadzetsa tsoka ndi imfayi, ndi kuswa malamulo a Mulungu — malamulo a cikondi. Komabe ngakhale pakati pa zobvuta zimene zimadza ci- fukwa ca zoipa, cikondi ca Mulungu cimaonekera. Zidalembedwa kuti Mulungu anatemberera nthaka cifukwa ca munthu. (Gen. 3: 17. ) Minga ndi mitula— mabvuto ndi mayeso, zimene zimacititsa moyo wace kukhala wa nchito ndi wa nkhawa — zinaperekedwa cifukwa ca ubwino wace, kuti zikhale za kumphunzitsa nzeru ya Mulungu ya kumtukula ku cionongeko ndi manyazi amene anadza ndi ucimo. Ngakhale dziko lidagwa si la cisoni cokha cokha. Mwa cilengedwe muli uthenga wa ciyembekezo ndi cisangalatso. Pa mitengo ya minga pali maluwa. Mau akuti “Mulungu ali cikondi,” alembedwa pa duwa liri lonse, ndi pa udzu uli wonse. Mbalame zimayimba nyimbo mokondwa mlengalenga, maluwa onunkhira, mitengo yobiriwira ya m’nkhalango, — zonse zimacitira umboni cisamaliro ca Atate Mulungu wathu ndi kuti Iye amafuna kukondwetsa ana ace. 5 6 MapaziOpitaKwaKristu Mau a Mulungu amaonetsa makhalidwe ace. Iye mwini ananena za cikondi cace ndi cifundo cace. Pamene Mose anapemphera, “Ndionetsenitu ulemerero wanu,” Yehova anayankha, “Ndidzapititsa ukoma wanga wonse pa maso pako.” (Eksodo 33: 18, 19. ) Uwu hdiwo ulemerero wace. Yehova anapita pa maso ya Mose, napfuula, [8] “Yehova, Yehova, Mulungu wa cifundo ndi wa cisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wocuruka, ndi wa coonadi; wa kusungira anthu osawerengeka cifundo, wakukhululukira mphulupulu ndi kulakwa ndi kucimwa.” (Eksodo 34: 6, 7. ) Iye “sasunga mkwiyo wace ku nthawi yonse popeza akondwera naco cifundo.” (Mika 7: 18. ) “Ndi woleka coipaco.” (Yona 4: 2. ) Mulungu anamangirira mitima yathu kwa Iye ndi zizindikiro zosawerengeka m’mwamba ndi m’dziko lapansi. Mulungu ana- funa kudziululira kwa ife kupyolera mwa nsinga za cilengedwe, zimene ziri nsinga zolimba za cikondi za dziko lapansi zimene mitima ya anthu ingazidziwe. Koma ngakhale zimenezi sizimaonet- sera kweni kweni za cikondi cace. Ngakhale mboni zonsezi zi- naperekedwa, mdani wa zabwino anadetsa mitima ya anthu kotero kuti anali kuyang’ana Mulungu ndi mantha; anamuganizira ngati woopsa wosakhululukira. Satana anatsogolera anthu kuganiza kuti Mulungu ali woweruza wa nkharwe, —amene zocita zace zonse ziri za ukari. Iye anamuganizira Mulungu ngati wakungoyang’anira ndi diso la nsanje kulonda zolakwa ndi zophophonya za anthu, kuti awalange. Yesu anadza kudzakhala pakati pa anthu kudzacotsa mdima umenewu pakusonyeza ku dziko lonse cikondi cosatha ca Mulungu. Mwana wa Mulungu anadza kucokera kumwamba kudzaonet- sera Atate. “Palibe munthu anaona Mulungu nthawi zonse; Mwana Wobadwa yekha wakukhala pa cifuwa ca Atate, Iyeyu anafotokoz- era.” (Yohane 1: 18. ) “Ndipo palibe wina adziwa Atate, koma Mwana yekha, ndi iye amene Mwana afuna kumuululira.” (Mateyu 11: 27. ) Pamene mmodzi wa akuphunzira anafunsa, “Tionetsereni Atate,” Yesu anayankha, “Kodi ndiri ndi inu nthawi yaikuru yotere, ndipo sunandizindikira Filipo? Iye amene wandiona Ine waona Atate, unena iwe bwanji, Mutionetsere Atate?” (Yohane 14: 8, 9. ) Pakufotokoza za nchito yace ya dziko lapansi, Yesu anati, “Iye anandidzoza Ine ndiuze anthu osauka Uthenga Wabwino, anan- dituma Ine kulalikira amnsinga mamasulidwe, ndi akhungu kuti

See more

The list of books you might like

Most books are stored in the elastic cloud where traffic is expensive. For this reason, we have a limit on daily download.